Leviticus 13:53 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Wansembe akaonetsetsa napeza kuti nguwiyo sidafalikire pa chovalacho, kapena pa chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembe akaona, ndipo taonani, nthenda njosakula pachovala, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma ngati wansembe akayangʼanitsitsa nguwiyo apeza kuti sinafalikire pa chovalacho kapena pa chinthu chilichonse chachikopa,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembe akaona, ndipo taonani, nthenda njosakula pacobvala, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa cinthu ciri conse copangika ndi cikopa;