Leviticus 13:55 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo wansembe achiwonetsetse chovala chimenecho chitachapidwa. Ngati banga la nguwiyo silidasinthe maonekedwe ake, ngakhale kuti siidafalikire, chovalacho nchoipitsidwa ndithu. Muchitenthe, osasamala zakuti banga la nguwiyo lili kumbuyo kapena kumaso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo wansembe aone nthenda ataitsuka, ndipo taonani, ngati nthendayi siinasandulika maonekedwe ake, yosakulanso nthenda, ndicho chodetsedwa; uchitenthe ndi moto; ndilo funka, kungakhale kuyera kwake kuli patsogolo kapena kumbuyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chovalacho chitachapidwa, wansembe achionenso ndipo ngati nguwiyo sinasinthe maonekedwe ake, ngakhale kuti sinafalikire, chovalacho ndi chodetsedwa ndithu. Muchitenthe, ngakhale kuti nguwiyo ili kumbuyo kapena kumaso kwa chinthucho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo wansembe aone nthenda ataitsuka, ndipo taonani, ngati nthendayi siinasandulika maonekedwe ace, yosakulanso nthenda, ndico codetsedwa; ucitenthe ndi moto; ndilo pfunka, kungakhale kuyera kwace kuli patsogolo kapena kumbuyo.