Leviticus 13:58 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma chovala, kapena chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, mukachapa, tsono nguwiyo nkuchoka, muchapenso kachiŵiri, ndipo chidzakhala choyeretsedwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ukatsuka chovalacho, kapena muyaro, kapena mtsendero, kapena chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa, ngati nthenda yalekapo pa chimenecho, achitsukenso kawiri, pamenepo chili choyera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chovala chathonje kapena chaubweya, ngakhale chinthu china chilichonse chopangidwa ndi chikopa, mukachichapa nguwi yake nʼkuchoka muchichapenso kawiri ndipo chidzakhala choyeretsedwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ukatsuka cobvalaco, kapena muyaro, kapena mtsendero, kapena cinthu ciri conse copangika ndi cikopa, ngati nthenda yalekapo pa cimeneco, acitsukenso kawiri, pamenepo ciri coyera.