Leviticus 13:59 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Limeneli ndi lamulo la nguwi yokhala pa chovala chaubweya kapena m'chovala chathonje, kapenanso m'chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, kuti muzisiyanitsa pakati pa chinthu choipitsidwa ndi chosaipitsidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ichi ndi chilamulo cha nthenda yakhate ili pa chovala chaubweya kapena chathonje, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa; kuchitcha choyera kapena kuchitcha chodetsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amenewa ndiwo malamulo a nguwi yokhala pa chovala chaubweya kapena pa chovala chathonje, kapenanso pa chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa kuti muzitha kulekanitsa choyeretsedwa ndi chodetsedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ici ndi cilamulo ca nthenda yakhate iri pa cobvala caubweya kapena cathonje, ngakhale pamuyare, kapena pamtsendero, kapena pa cinthu ciri conse copangika ndi cikopa; kucicha coyera kapena kucicha codetsa.