Leviticus 13:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono wansembe uja amuwonetsetsenso wodwalayo pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Pakhungu pakakhala pothimbirira, nthendayo yosafalikira pakhungupo, wansembe amutchule munthuyo kuti ndi wosaipitsidwa. Umenewo ndi m'buko chabe, tsono wodwalayo achape zovala zake, ndipo adzakhala woyeretsedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo wansembe amuonenso tsiku lachisanu ndi chiwiri, ndipo taonani, nthenda yazimba yosapitirira khungu nthendayi, pamenepo wansembe amutche iye woyera, ndiyo nkhanambo chabe; ndipo atsuke zovala zake, ndiye woyera;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembeyo amuonenso bwino munthuyo, ndipo ngati nthendayo yazima ndi kusafalikira pa khungu, wansembe amutchule munthuyo kuti ndi woyera. Umenewo unali mʼbuko chabe. Choncho munthuyo achape zovala zake ndipo adzakhala woyera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo wansembe amuonenso tsikulacisanu ndi ciwiri, ndipo taonani, nthenda yazimba yosapitirira khungu nthendayi, pamenepo wansembe amuche iye woyera, ndiyo nkhanambo cabe; ndipo atsuke zobvala zace, ndiye woyera;