Leviticus 14:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, wodwalayo atenge anaankhosa amphongo aŵiri opanda chilema, atengenso mwanawankhosa mmodzi wamkazi, wa chaka chimodzi, wopanda chilema, ndi chochepereka cha chakudya wosalala wolemera makilogaramu atatu, wosakaniza ndi mafuta, ndiponso mafuta okwanira limodzi mwa magawo atatu a lita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge anaankhosa awiri, amuna opanda chilema, ndi mwanawankhosa mmodzi wamkazi wa chaka chimodzi wopanda chilema, ndi atatu a magawo khumi a efa la ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndi muyeso umodzi wa magawo atatu wa mafuta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pa tsiku lachisanu ndi chitatu munthuyo atenge ana ankhosa aamuna awiri ndi mwana wankhosa wamkazi wa chaka chimodzi. Zonsezi zikhale zopanda chilema. Atengenso chopereka chachakudya cha ufa wosalala wa makilogalamu atatu wosakaniza ndi mafuta wokwana limodzi mwa magawo atatu a lita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsiku lacisanu ndi citatu atenge ana a nkhosa awiri, amuna opanda cirema, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamkazi wa caka cimodzi wopanda cirema, ndi atatu a magawo khumi a ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndi muyeso umodzi wa mafuta.