Leviticus 14:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wansembe atengeko mwanawankhosa wamphongo mmodzi ndi kumpereka kuti akhale nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta aja. Aziweyule, kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo wansembe atenge mwanawankhosa mmodzi wamwamuna, nabwere naye akhale nsembe yopalamula, pamodzi ndi muyeso uja wa mafuta, naziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo wansembe atenge mwana wankhosa wamwamuna mmodzi ndi kumupereka kuti akhale nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta wokwana limodzi mwa magawo atatu a lita. Wansembe aziweyule zonsezi pamaso pa Yehova kuti zikhale chopereka choweyula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo wansembe atenge mwana wa nkhosa mmodzi wamwamuna, nabwere naye akhale nsembe yoparamula, pamodzi ndi muyeso uja wa mafuta, naziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.