Leviticus 14:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwanawankhosayo amuphere pamalo pomwe amaphera nyama yoperekera nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yopsereza, ndiye kuti pa malo oyera aja, pakuti chopereka chopepesera kupalamula ndi chake cha wansembe, monga momwe chimakhalira chopereka chopepesera machimo. Zoperekazo nzoyera kopambana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akaphere mwanawankhosa wamwamuna paja amapherapo nsembe yauchimo, ndi nsembe yopsereza, pa malo popatulika; pakuti monga nsembe yauchimo momwemo nsembe yopalamula nja wansembe; ndiyo yopatulika kwambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwana wankhosayo amuphere pa malo amene amaphera nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yopsereza, kutanthauza malo opatulika. Monga zimakhalira ndi chopereka chopepesera machimo, chopereka ichi ndi chake cha wansembe ndipo ndi chopereka choyera kopambana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akaphere mwana wa nkhosa wamwamuna paja amapherapo nsembe yaucimo, ndi nsembe yopsereza, pa malo popatulika; pakuti monga nsembe yaucimo momwemo nsembe yoparamula, nja wansembe; ndiyo yopatulikitsa.