Leviticus 14:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo aviike chala chake cha ku dzanja lamanja m'mafuta amene ali m'dzanja lakumanzerewo, ndi kuwazako mafutawo ndi chala chake kasanu ndi kaŵiri pamaso pa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo wansembe aviike chala chake cha dzanja lake lamanja cha iye mwini m'mafuta ali m'dzanja lake lamanzere, nawaze mafuta kasanu ndi kawiri ndi chala chake pamaso pa Yehova;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
aviyike chala chake cha ku dzanja lamanja mʼmafuta amene ali mʼdzanja lamanzerewo, ndi kuwaza mafutawo ndi chala chakecho kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo wansembe abviike cala cace ca dzanja lace lamanja ca iye mwini m'mafuta ali m'dzanja lace lamanzere, nawaze mafuta kasanu ndi kawiri ndi cala cace pamaso pa Yehova;