Leviticus 14:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mafuta otsala m'dzanja la wansembeyo, aŵapakeko pa nsonga ya khutu la ku dzanja lamanja la munthu woyeretsedwa uja, ndiponso pa chala chake chachikulu cha ku dzanja lamanja. Aŵapakenso pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja, pamalo pamene anali atapaka magazi aja a nyama yoperekera nsembe yopepesera kupalamula ija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo wansembe apakeko mafuta okhala m'dzanja lake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja, pa mwazi wa nsembe yopalamula;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembe apake mafuta otsala mʼdzanja lake pa khutu lakumanja la munthu amene akuyeretsedwayo. Awapakenso pa chala chake chachikulu cha ku dzanja lamanja ndiponso pa chala chake chachikulu cha ku phazi lakumanja, pamalo pamene anali atapakapo magazi a nsembe yopepesera kupalamula paja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo wansembe apakeko mafuta okh a ria m'dzanja lace pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa cala cacikuru ca dzanja lace lamanja, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja, pa mwazi wa nsembe yoparamula;