Leviticus 14:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake wansembe apereke nsembe yopepesera machimo, kuti achite mwambo wompepesera munthu woti ayeretsedwe khate lake uja. Kenaka wansembeyo aphe nyama yoperekera nsembe yopsereza,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembe apereke nsembe yauchimo, namchitire chomtetezera amene akuti ayeretsedwe, chifukwa cha kudetsedwa kwake; ndipo atatero aphe nsembe yopsereza;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kenaka wansembe apereke nsembe yopepesera machimo kuti achite mwambo womupepesera munthu woti ayeretsedwe khate lake uja. Atatha kuchita zimenezi, wansembe aphe nyama ya nsembe yopsereza
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembe apereke nsembe yaucimo, namcitire comtetezera amene akuti ayeretsedwe, cifukwa ca kudetsedwa kwace; ndipo atatero aphe nsembe yopsereza;