Leviticus 14:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma munthu wodwalayo akakhala wosauka, kuti alibe zonsezo, apereke mwanawankhosa wamphongo kuti akhale nsembe yopepesera kupalamula. Aipereke moweyula manja, kuti achite mwambo wompepesera. Aperekenso kilogaramu limodzi la ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, kuti ukhale nsembe yaufa, pamodzi ndi mafuta okwanira limodzi mwa magawo atatu a lita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akakhala waumphawi chosafikana chuma chake azitenga mwanawankhosa mmodzi wamwamuna akhale nsembe yopalamula, aiweyule kumchitira chomtetezera, ndi limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa, ndi muyeso umodzi magawo atatu wa mafuta;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ngati munthu woti ayeretsedweyo ndi wosauka ndipo sangathe kupeza zinthu zimenezi, apereke mwana wankhosa wamwamuna monga nsembe yopepesera kupalamula ndipo ayiweyule pochita mwambo womupepesera. Aperekenso kilogalamu imodzi ya ufa wosalala osakaniza ndi mafuta kuti ikhale nsembe yachakudya, pamodzi ndi mafuta wokwanira limodzi mwa magawo atatu a lita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akakhala waumphawi cosafikana cuma cace azitenga mwana wa nkhosa mmodzi wamwamuna akhale nsembe yoparamula, aiweyule kumcitira comtetezera, ndi limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa, ndi muyeso umodzi wa mafuta;