Leviticus 14:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aperekenso njiŵa ziŵiri kapena maundaankhunda aŵiri, monga m'mene angathere. Imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo, inayo ikhale ya nsembe yopsereza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, monga akhoza kufikana; limodzi likhale la nsembe yauchimo, ndi linzake la nsembe yopsereza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aperekenso njiwa ziwiri kapena mawunda awiri zomwe iye angathe kuzipeza. Imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo, ndi inayo ikhale ya nsembe yopsereza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, monga akhoza kufikana; limodzi likhale la nsembe yaucimo, ndi linzace la nsembe yopsereza.