Leviticus 14:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono nkhosa yoperekera nsembe yopepesera kupalamulayo aiphe. Atengeko magazi ake ndi kuŵapaka pa nsonga ya khutu la ku dzanja lamanja la munthu amene ayeretsedweyo, ndi pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, pamodzi ndi pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
naphe mwanawankhosa wa nsembe yopalamula, ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yopalamula, naupake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye akuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembe aphe nkhosa yopereka nsembe yopepesera kupalamula ndipo atenge magazi ake ndi kuwapaka pa msonga ya khutu lakumanja la munthu amene ayeretsedweyo. Awapakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndiponso pa chala chachikulu cha ku phazi lakumanja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
naphe mwana wa nkhosa wa nsembe yoparamula, ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yoparamula, naupake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye akuti ayeretsedwe, ndi pa cala cacikuru ca dzanja lace lamanja, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja;