Leviticus 14:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apakekonso mafuta omwewo pa nsonga ya khutu la ku dzanja lamanja la munthu amene ayeretsedweyo. Aŵapakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja pamodzi ndi pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja, pamalo pomwe anali atapaka magazi a nyama yoperekera nsembe yopepesera kupalamula ija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo wansembe apakeko mafuta aja ali m'dzanja lake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja, pa malo paja pali mwazi wa nsembe yopalamula;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Apakenso mafuta omwewo amene ali mʼdzanja lake lamanja pa msonga ya khutu la kudzanja lamanja la munthu amene akuyeretsedwayo. Apakenso pa chala chachikulu cha phazi lakumanja, pamalo pamene anapakapo magazi a nsembe yopepesera kupalamula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo wansembe apakeko mafuta aja ali m'dzanja lace pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa cala cacikuru ca: dzanja lace lamanja, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja, pa malo paja pali mwazi wa usembe yoparamula;