Leviticus 14:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono wansembe asanawonetsetse nderezo, alamule kuti anthu atulutse zinthu zonse m'nyumbamo, kuti zam'nyumbazo angazitchule kuti nzoipitsidwa. Pambuyo pake wansembeyo aloŵe m'nyumbamo kuti aonemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembe aziuza kuti atulutse zonse za m'nyumba, asanalowe kudzaona nthendayi, zinthu zonse zili m'nyumba zingakhale zodetsedwa; ndipo atatero wansembe alowe kukaona nyumbayi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono wansembe alamule kuti anthu atulutse zinthu zonse mʼnyumbamo iye asanalowemo ndi kukaonetsetsa ndereyo kuti mʼnyumbamo musapezeke chinthu choti achitchule chodetsedwa. Izi zitachitika, wansembe alowe mʼnyumbamo ndi kukaonamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembe aziuza kuti aturutse zonse za m'nyumba, asanalowe kudzaona nthendayi, zinthu zonse ziri m'nyumba zingakhale zodetsedwa; ndipo atatero wansembe alowe kukaona nyumbayi;