Leviticus 14:48 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma wansembe akabwera naonetsetsa m'nyumbamo ndi kupeza kuti nthendayo sidafalikiremo, nyumbayo ataimata kale, wansembe aitchule nyumbayo kuti njosaipitsidwa, poti nderezo mulibe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembe akalowa, nakaona, ndipo taonani, nthenda siinakula m'nyumba, ataimata nyumba; wansembe aitche nyumbayo yoyera, popeza nthenda yaleka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma ngati pambuyo pa kuyimata, wansembe abwera kudzaonetsetsa mʼnyumbamo napeza kuti ndereyo sinafalikire, iye alengeze kuti nyumbayo ndi yoyeretsedwa, chifukwa ndereyo yatha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembe akalowa, nakaona, ndipo taonani, nthenda siinakula m'nyumba, ataimata nyumba; wansembe aiche nyumbayo yoyera, popeza nthenda yaleka.