Leviticus 14:51 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka atenge nthambi yamkungudza, kachitsamba ka hisope, ndi kansalu kamlangali, pamodzi ndi kambalame kamoyo kaja, zonsezo aziviike m'magazi a kambalame kophedwa kaja, ndiponso m'madzi atsopano aja, ndipo awaze nyumbayo kasanu ndi kaŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
natenge mtengo wamkungudza ndi hisope, ndi ubweya wofiira, ndi mbalame yamoyo, naziviike m'mwazi wa mbalame yakuphayo, ndi m'madzi oyenda, nawaze kasanu ndi kawiri m'nyumba;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka atenge kanthambi kamkungudza, kachitsamba ka hisope, kansalu kofiirira pamodzi ndi mbalame yamoyo ija, zonsezi aziviyike mʼmagazi a mbalame yophedwa ija, ndiponso mʼmadzi abwino aja, ndipo awaze nyumbayo kasanu ndi kawiri
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
natenge mtengo wamkungudza ndi hisope, ndi ubweya wofiira, ndi mbalame yamoyo, nazibviike m'mwazi wa mbalame yakuphayo, ndi m'madzi oyenda, nawaze kasanu ndi kawiri m'nyumba;