Leviticus 14:52 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atatero, ndiye kuti wansembeyo waiyeretsa nyumbayo ndi magazi a mbalame, madzi atsopano, mbalame yamoyo, nthambi yamkungudza, kachitsamba ka hisope, ndiponso kansalu kamlangali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nayeretse nyumba ndi mwazi wa mbalame, ndi madzi oyenda, ndi mbalame yamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akatero ndiye kuti wayeretsa nyumbayo ndi magazi a mbalame, madzi abwino, mbalame yamoyo, kanthambi kamkungudza, kachitsamba ka hisope ndi kansalu kofiirira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nayeretsenyumbandi mwazi wa mbalame, ndi madzi oyenda, ndi mbalame yamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira.