Leviticus 14:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wansembe atenge mbalame yamoyo ija pamodzi ndi nthambi yamkungudza ija, kansalu kamlangali kaja ndi kachitsamba ka hisope kaja. Zonsezo pamodzi ndi mbalame yamoyoyo, aziviike m'magazi a mbalame yomwe adaiphera m'mbale pamwamba pa madzi atsopano ija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
natenge mbalame yamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, naziviike pamodzi ndi mbalame yamoyo m'mwazi wa mbalame adaipha pamwamba pa madzi oyenda;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka wansembe atenge mbalame yamoyo ija ndi kuyinyika pamodzi ndi nthambi yamkungudza, kansalu kofiirira ndi kanthambi ka hisope kaja mʼmagazi ambalame imene anayiphera pamwamba pa madzi abwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
natenge nbalame yamoyo, ndi mtengo wankungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, nazibviike pamodzi ndi mbalame yamoyo m'mwazi wa mbalame adaipha pamwamba pa madzi oyenda;