Leviticus 15:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Munthu wotulutsa mafinyayo akaona kuti wachira, aŵerenge masiku asanu ndi aŵiri a kuyeretsedwa kwake, kenaka achape zovala zake, asambe pa kasupe, ndipo adzakhala woyeretsedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wakukhayo atayeretsedwa ku kukha kwake, adziwerengere masiku asanu ndi awiri akhale a kuyeretsa kwake, natsuke zovala zake; nasambe thupi lake ndi madzi oyenda, nadzakhala woyera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Munthu wotulutsa mafinyayo akaona kuti wachira, awerenge masiku asanu ndi awiri akuyeretsedwa kwake kenaka achape zovala zake ndi kusamba pa kasupe, ndipo adzayeretsedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wakukhayo atayeretsedwa ku kukha kwace, adziwerengere masiku asanu ndi awiri akhale a kuyeretsa kwace, natsuke zobvala zace; nasambe thupi lace ndi madzi oyenda, nadzakhala woyera.