Leviticus 15:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mkazi akakhala wosamba, ndipo ikakhala nthaŵi yeniyeni yakusamba, akhala woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri, aliyense amene amkhudze akhala woipitsidwa mpaka madzulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ngati mkazi ali ndi nthenda yakukha, ndi kukha kwake nkwa mwazi m'thupi mwake, akhale padera masiku asanu ndi awiri; ndipo aliyense amkhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Mkazi akakhala wosamba ndipo ikakhala kuti ndi nthawi yake yeniyeni yosamba, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri. Aliyense amene adzamukhudza adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ngati mkazi ali ndi nthenda yakukha, ndi kukha kwace nkwa mwazi m'thupi mwace, akhale padera masiku asanu ndi awiri; ndipo ali yense amkhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.