Leviticus 15:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwamuna aliyense akagona ndi mkazi amene akusambabe, mwamunayo akhala woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri. Ndipo bedi lililonse limene mwamunayo agonepo likhala loipitsidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ngati mwamuna aliyense agona naye, ndi kudetsa kwake kukhala pa iye, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri; ndipo kama aliyense agonapo ali wodetsedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Mwamuna aliyense akagona naye ndipo magazi osamba kwake ndi kumukhudza, munthuyo adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri, ndipo bedi limene wagonapo lidzakhalanso lodetsedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ngati mwamuna ali yense agona naye, ndi kudetsa kwace kukhala pa iye, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri; ndipo kama ali yense agonapo ali wodetsedwa.