Leviticus 15:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mkazi akataya magazi masiku ambiri osakhala nthaŵi yake yosamba, kapena akamasambabe kupitirira pa nthaŵi yake ya kusamba, masiku onsewo mkaziyo ali wotaya magazi ndi woipitsidwa, monga momwe amakhalira pa masiku ake osamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkazi akakhala ndi kukha mwazi masiku ambiri, osati masiku a kuoloka kwake, kapena akamakha kupitirira nthawi ya kuoloka kwake; masiku onse chilinkukha chomdetsa chake, adzakhala wodetsedwa, monga masiku a kuoloka kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Mkazi akataya magazi masiku ambiri, wosakhala pa nthawi yake yosamba, kapena akamasambabe kupitirira nthawi yake yosamba, mkaziyo adzakhala wodetsedwa nthawi yonse imene akutaya magazi, monga momwe amakhalira pa masiku ake osamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkazi akakhala ndi kukha mwazi masiku ambiri, osati masiku a kuoloka kwace, kapena akamakha kupitirira nthawi ya kuoloka kwace; masiku onse cirinkukha comdetsa cace, adzakhala wodetsedwa, monga masiku a kuoloka kwace.