Leviticus 15:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bedi lililonse limene mkaziyo agonepo pa masiku onse pamene ali wotaya magazi, lidzakhala loipitsidwa. Ndipo zonse zimene amakhalirapo zikhala zoipitsidwa, monga momwe zimakhalira zoipitsidwa pamene ali wosamba pa nthaŵi yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kama aliyense agonapo masiku a kukha kwake akhale ngati kama wa kuoloka kwake; ndi chinthu chilichonse akhalapo chili chodetsedwa, ngati kudetsa kwa kuoloka kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Bedi lililonse limene mkaziyo adzagonapo pa masiku onse pamene ali wotaya magazi, ndiponso chilichonse chimene wakhalira chidzakhala chodetsedwa monga mmene chimakhalira chodetsedwa pa nthawi yake yosamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kama ali yense agonapo masiku a kukha kwace akhale ngati kama wa kuoloka kwace; ndi cinthu ciri conse akhalapo ciri codetsedwa, ngati kudetsa kwa kuoloka kwace.