Leviticus 15:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aliyense wokhudza zimenezi akhala woipitsidwa. Tsono achape zovala zake ndi kusamba thupi lonse, koma akhala woipitsidwabe mpaka madzulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu aliyense akakhudza zimenezi adzakhala wodetsedwa, natsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense amene adzakhudza zinthu zimenezo adzakhala wodetsedwa ndipo ayenera kuchapa zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu ali yense akakhudza zimenezi adzakhala wodetsedwa, natsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.