Leviticus 15:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wansembe apereke imodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ndipo ina ikhale nsembe yopsereza. Akatero, ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera mkaziyo pamaso pa Chauta, chifuwa cha matenda ake osamba aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembe apereke limodzi likhale nsembe yauchimo, ndi linalo likhale nsembe yopsereza; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova chifukwa cha kukha kwake komdetsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembe apereke imodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza. Pamenepo ndiye kuti wansembeyo wachita mwambo wopepesera mkaziyo pamaso pa Yehova chifukwa cha matenda ake wosamba aja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembe apereke limodzi likhale nsembe yaucimo, ndi linalo likhale nsembe yopsereza; ndipo wansembe amcitire comtetezera pamaso pa Yehova cifukwa ca kukha kwace komdetsa.