Leviticus 15:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Choncho mudzaŵayeretsa Aisraele m'kuipitsidwa kwao, kuti angafe chifukwa chochita tchimo la kudetsa chihema changa, chimene chili pakati pao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Motero muzipatula ana a Israele kwa kudetsedwa kwao; angafe m'kudetsedwa kwao, pamene adetsa Kachisi wanga ali pakati pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Choncho muwayeretsa ana a Israeli nʼkudetsedwa kwawo kuti angafe pochita tchimo lowadetsa limene polichita limadetsa malo anga wokhalamo amene ali pakati pawo.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Motero muzipatula ana a Israyeli kwa kudetsedwa kwao; angafe m'kudetsedwa kwao, pamene adetsa kacisi wanga ali pakati pao.