Leviticus 16:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi ya Azazele, abwere nayo yamoyo pamaso pa Chauta, kuti achite mwambo wopepesera machimo pa mbuziyo, ndi kuitumiza ku chipululu kwa Azazele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mbuzi imene adaigwera maere a Azazele, aiike yamoyo pamaso pa Yehova, kuti achite nayo chotetezera, kuitumiza kuchipululu ikhale ya Azazele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi yosenza machimo, apereke ya moyo pamaso pa Yehova, kuti achite mwambo wopepesera machimo pa mbuziyo poyitumiza ku chipululu kuti ikhale ya Azazele.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mbuzi imene adaigwera maere a Azazeli, aiike yamoyo pamaso pa Yehova, kuti acite nayo cotetezera, kuitumiza kucipululu ikhale ya Azazeli.