Leviticus 16:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka atenge kambiya kodzaza ndi makala a moto ochokera pa guwa lansembe pamaso pa Chauta, atape lubani wonunkhira ndi woperapera, manja aŵiri, ndipo aloŵe naye kuseri kwa nsalu yochinga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
natenge mbale ya zofukiza yodzala ndi makala amoto, kuwachotsa pa guwa la nsembe, pamaso pa Yehova, ndi manja ake odzala ndi chofukiza chopera cha fungo lokoma, nalowe nayo m'tseri mwa nsalu yotchinga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka iye atenge chofukizira chodzaza ndi makala a moto ochokera pa guwa lansembe pamaso pa Yehova. Atengenso lubani wonunkhira ndi woperapera wokwanira manja awiri, ndipo alowe naye kuseri kwa katani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
natenge mbale ya zofukiza yodzala ndi makara amoto, kuwacotsa pa guwa la nsembe, pamaso pa Yehova, ndi manja ace odzala ndi cofukiza copera ca pfungo lokoma, nalowe nayo m'tseri mwa nsaru yocinga;