Leviticus 16:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka atengeko magazi ena a ng'ombeyo, aŵawaze ndi chala chake pa chivundikiro cha bokosi lachipangano mbali yakuvuma. Ndiponso awazeko magaziwo kasanu ndi kaŵiri ndi chala chake patsogolo pa chivundikirocho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi kuuwaza ndi chala chake pachotetezerapo, mbali ya kum'mawa; nawaze mwazi ndi chala chake chakuno cha chotetezerapo kasanu ndi kawiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo atenge magazi ena a ngʼombeyo, awawaze ndi chala chake pa chivundikiro cha kummawa; kenaka awaze magaziwo ndi chala chake kasanu ndi kawiri patsogolo pa chivundikirocho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi kuuwaza ndi cala cace pacotetezerapo, mbali ya kum'mawa; nawaze mwazi ndi cala cace cakuno ca cotetezerapo kasanu ndi kawiri.