Leviticus 16:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono Aroni aphe mbuzi ya nsembe yopepesera machimo a anthu. Magazi ake aloŵe nawo kuseri kwa nsalu yochinga, ndi kuchita nawo monga momwe adachitira ndi magazi a ng'ombe, pakuwaza magaziwo pa chivundikiro chija ndi patsogolo pa chivundikirocho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo aiphe mbuzi ya nsembe yauchimo, ndiyo yophera anthu, nalowe nao mwazi wake m'tseri mwa nsalu yotchinga, nachite nao mwazi wake monga umo anachitira ndi mwazi wa ng'ombe, nauwaze pachotetezerapo ndi chakuno cha chotetezerapo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kenaka Aaroni aphe mbuzi ya nsembe yopepesera machimo a anthu, ndipo magazi ake alowe nawo kuseri kwa katani ndi kuchita chimodzimodzi monga anachitira ndi magazi a ngʼombe aja: Aaroni awaze magaziwo pa chivundikiro chija ndi patsogolo pa chivundikirocho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo aiphe mbuzi ya nsembe yaucimo, ndiyo yophera anthu, nalowe nao mwazi wace m'tseri mwa nsaru yocinga, nacite nao mwazi wace monga umo anacitira ndi mwazi wa ng'ombe, nauwaze pacotetezerapo ndi cakuno ca cotetezerapo;