Leviticus 16:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono atatuluka Aroniyo apite ku guwa limene lili pamaso pa Chauta ndi kulichitira mwambo wolipepesera. Atengeko magazi a ng'ombe yamphongo ndiponso a mbuzi, ndi kuŵapaka pa nyanga za guwalo molizungulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atulukire guwa la nsembe lokhala pamaso pa Yehova ndi kulichitira chotetezera; natengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi mwazi wa mbuziyo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kenaka, Aaroniyo akatuluka apite ku guwa limene lili pamaso pa Yehova ndi kulichitira mwambo wolipepesera. Atengeko magazi a ngʼombe yayimuna ndiponso magazi a mbuzi ndi kuwapaka pa nyanga zonse za guwa lansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo aturukire guwa la nsembe lokhala pamaso pa Yehova ndi kulicitira cotetezera; natengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi mwazi wa mbuziyo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira.