Leviticus 16:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aroni mbale wako kuti asamaloŵa nthaŵi iliyonse ku malo opatulika kwambiri, kuseri kwa nsalu yochinga, pamaso pa chivundikiro chokhala pamwamba pa Bokosi lachipangano, kuti angafe, chifukwa Ine ndidzaonekera mu mtambo pamwamba pa chivundikirocho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m'malo opatulika m'tseri mwa nsalu yotchinga, pali chotetezerapo chokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pachotetezerapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anawuza Mose kuti, “Uza mchimwene wako Aaroni kuti asamalowe ku Malo Wopatulika, kuseri kwa katani, pamaso pa chivundikiro cha Bokosi la Chipangano nthawi iliyonse imene akufuna kuopa kuti angadzafe, pakuti Ine ndimaoneka mu mtambo umene uli pamwamba pa chivundikiro cha Bokosi la Chipangano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m'malo opatulika m'tseri mwa nsaru yocinga, pali cotetezerapo cokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pacotetezerapo.