Leviticus 16:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aroni asanjike manja ake pamutu pa mbuziyo, ndipo aululire pa mbuzi imeneyo zochimwa zonse za Aisraele pamodzi ndi kusamvera kwao konse, ndiye kuti machimo ao onse. Machimowo aŵaike pamutu pa mbuzi ija, ndipo munthu amene adamusankhiratu aithamangitsire ku chipululu mbuziyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo Aroni aike manja ake onse awiri pamutu pa mbuzi yamoyo, ndi kuvomereza pa iyo mphulupulu zonse za ana a Israele, ndi zolakwa zao zonse, monga mwa zochimwa zao zonse; naike izi pamutu pa mbuziyo, ndi kuitumiza kuchipululu ndi dzanja la munthu wompangiratu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aaroni asanjike manja ake pa mutu wa mbuziyo ndipo awulule pa mbuziyo zoyipa zonse ndi zowukira zonse za Aisraeli, kutanthauza machimo awo onse. Machimowo awayike pa mutu wa mbuziyo. Kenaka munthu amene anasankhidwa athamangitsire mbuziyo ku chipululu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo Aroni aike manja ace onse awiri pamutu pa mbuzi yamoyo, ndi kubvomereza pa iyo mphulupulu zonse za ana a Israyeli, ndi zolakwa zao zonse, monga mwa zocimwa zao zonse; naike izi pamutu pa mbuziyo, ndi kuitumiza kucipululu ndi dzanja la munthu wompangiratu,