Leviticus 16:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Asambe thupi lonse ku malo oyera, ndipo avale zovala zake. Atuluke kukapereka nsembe yopsereza ya iye mwini, ndiponso nsembe yopsereza yoperekera anthu. Akatero, ndiye kuti wachita mwambo wopepesera machimo a iye mwini ndi a anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo asambe thupi lake ndi madzi kumalo kopatulika, navale zovala zake, natuluke, napereke nsembe yopsereza yake, ndi nsembe yopsereza ya anthu, nachite chodzitetezera yekha ndi anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Asambe thupi lonse ku Malo Wopatulika ndi kuvala zovala zake za nthawi zonse. Kenaka atuluke ndi kukapereka nsembe yopsereza ya iye mwini, ndiponso nsembe yopsereza yoperekera anthu. Akatero ndiye kuti wachita mwambo wopepesera machimo a iye mwini wake ndi a anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo asambe thupi lace ndi madzi kumalo kopatulika, nabvale zobvala zace, naturuke, napereke nsembe yopsereza yace, ndi nsembe yopsereza ya anthu, nacite codzitetezera yekha ndi anthu.