Leviticus 16:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ng'ombe ndi mbuzi zoperekera nsembe zopepesera machimo zija, zimene magazi ake adabwera nawo kuti achitire mwambo wopepesera malo oyera, azitulutsire kunja kwa zithando. Zikopa zake, nyama yake ndi ndoŵe yake azitenthe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndi mbuzi ya nsembe yauchimo, zimene mwazi wao analowa nao kuchita nao chotetezera m'malo opatulika, atuluke nazo kunja kwa chigono; natenthe ndi moto zikopa zao, ndi nyama zao, ndi chipwidza chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngʼombe ndi mbuzi zoperekera nsembe yopepesera machimo zimene magazi ake anabwera nawo kuti achitire mwambo wopepesera Malo Wopatulika, azitulutsire kunja kwa msasa. Koma zikopa zake, nyama yake ndi matumbo ake azitenthe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ng'ombe ya nsembe yaucimo, ndi mbuzi ya nsembe yaucimo, zimene mwazi wao analowa nao kucita nao cotetezera m'malo opatulika, aturuke nazo kunja kwa cigono; natenthe ndi mota zikopa zao, ndi nyama zao, ndi cipwidza cao.