Leviticus 16:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Limeneli likhale lamulo lanu lamuyaya kuti mwezi wachisanu ndi chiŵiri, pa tsiku lakhumi la mwezi, muzisala zakudya ndipo musagwire ntchito iliyonse, inu mbadwa, ndiponso mlendo wokhala nao pakati panu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo lizikhala kwa inu lemba losatha; mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi la mweziwo, muzidzichepetsa, osagwira ntchito konse, kapena wa m'dziko, kapena mlendo wakukhala pakati panu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ili likhale lamulo lanu lamuyaya: Mwezi wachisanu ndi chiwiri, pa tsiku la khumi la mwezi, mugonje pamaso pa Yehova. Musamagwire ntchito iliyonse, kaya ndinu mbadwa kapena mlendo amene akukhala pakati panu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo lizikhala kwa Inu lemba Ilosatha; mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku lakhumi la mweziwo, muzidzicepetsa, osagwira Debito konse, kapena wa m'dziko, kapena mlendo wakukhala pakati panu;