Leviticus 16:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wansembe amene wadzozedwa nayeretsedwa kuti akhale mkulu wa ansembe onse m'malo mwa bambo wake, adzachite mwambo wopepesera machimo, atavala zovala zopatulika zabafuta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembe, amene anamdzoza ndi kumdzaza dzanja lake achite ntchito ya nsembe m'malo mwa atate wake, achite chotetezera, atavala zovala zabafuta, zovala zopatulikazo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembe amene wadzozedwa ndi kupatulidwa kuti akhale wansembe kulowa mʼmalo mwa abambo ake ndiye azichita mwambo wopepesera machimo atavala zovala zake zosalala ndi zopatulika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembe, amene anamdzoza ndi kumdzaza dzanja lace acite nchito ya nsembe m'malo mwa atate wace, acite cotetezera, atabvala zobvala zabafuta, zobvala zopatulikazo.