Leviticus 16:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Limeneli lidzakhala lamulo lanu lamuyaya, kuti muzidzachita mwambo wopepesera machimo onse a Aisraele kamodzi pa chaka.” Tsono Mose adachita monga momwe Chauta adamlamulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ichi chikhale kwa inu lemba losatha, kuchita chotetezera ana a Israele, chifukwa cha zochimwa zao zonse, kamodzi chaka chimodzi. Ndipo anachita monga Yehova adauza Mose.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ili likhale lamulo lanu lamuyaya. Mwambo wopepesera machimo uzichitika kamodzi pa chaka chifukwa cha machimo a anthu onse.” Ndipo Mose anachita monga momwe Yehova analamulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ici cikhale kwa inu lemba losatha, kucita cotetezera ana a Israyeli, cifukwa ca zocimwa zao zonse, kamodzi caka cimodzi. Ndipo anacita monga Yehova adauza Mose.