Leviticus 16:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Azivala mwinjiro woyera wabafuta, azivalanso kabudula wabafuta ndi kumangira lamba wabafuta, ndipo avalenso nduŵira yabafuta kumutu. Zimenezi ndi zovala zopatulika. Avale zimenezi atasamba thupi lonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Avale malaya a m'kati a bafuta wopatulika, nakhale nazo zovala za kumiyendo pathupi pake, nadzimangire m'chuuno ndi mpango wabafuta, navale nduwira yabafuta; izi ndi zovala zopatulika; potero asambe thupi lake ndi madzi, ndi kuvala izi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Azivala mwinjiro wopatulika wa nsalu yosalala, azivalanso kabudula wa mʼkati wa nsalu yosalala, azimanga lamba wa nsalu yosalala, ndipo avalenso nduwira ya nsalu yosalala kumutu. Zimenezi ndi nsalu zopatulika ndipo atasamba thupi lonse azivala zimenezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Abvale maraya a m'kati a bafuta wopatulika, nakhale nazo zobvala za kumiyendo pathupi pace, nadzimangire m'cuuno ndi mpango wabafuta, nabvale nduwira yabafuta; izi ndi zobvala zopatulika; potero asambe thupi lace ndi madzi, ndi kubvala izi.