Leviticus 17:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mwisraele aliyense, kapena mlendo wokhala pakati pao, akadya magazi, ndidzamfulatira ndi kumchotsa pakati pa anthu anzake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu aliyense wa mbumba ya Israele, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uliwonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mwisraeli aliyense kapena mlendo aliyense wokhala pakati panu amene adya magazi, ndidzamufulatira ndipo ndidzamuchotsa pakati pa anthu anzake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu ali yense wa mbumba ya Israyeli, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uli wonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumcotsa kwa anthu a mtundu wace.