Leviticus 17:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti moyo wake wa cholengedwa chilichonse uli m'magazi, ndipo ndaŵapereka kwa inu kuti muzichitira mwambo wopepesera machimo a moyo wanu pa guwa. Pajatu magazi ndiwo amene amachotsa machimo, chifukwa cha moyo umene umakhala m'magazimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti moyo wa nyama ukhala m'mwazi; ndipo ndakupatsani uwu pa guwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu; pakuti wochita chotetezera ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti moyo wa cholengedwa chilichonse uli mʼmagazi, ndipo ndawupereka kwa inu kuti muzichitira mwambo wopepesera machimo a moyo wanu pa guwa. Pajatu magazi ndiwo amachotsa machimo chifukwa moyo uli mʼmenemo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti moyo wa nyama ukhala m'mwazi; ndipo ndakupatsani uwu pa guwa la nsembe, ucite cotetezera moyo wanu; pakuti wocita cotetezera ndiwo mwazi, cifukwa ca moyo wace.