Leviticus 17:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Aisraele onse kapena alendo okhala pakati pao, amene amapha ku uzimba nyama kapena mbalame zimene amadya, ataye magazi ake pansi ndi kuŵakwirira ndi dothi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu aliyense wa ana a Israele, kapena mlendo wakugonera pakati pa inu, akasaka nyama kapena mbalame yakudya, nakaigwira; azikhetsa mwazi wake, naufotsere ndi dothi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mwisraeli aliyense kapena mlendo aliyense wokhala pakati panu amene amasaka ndi kupha nyama zakuthengo kapena mbalame zimene amadya, ataye magazi ake pansi ndi kuwakwirira ndi dothi,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu ali yense wa ana a Israyeli, kapena mlendo wakugonera pakati pa inu, akasaka nyama kapena mbalame yakudya, nakaigwira; azikhetsa mwazi wace naufotsere ndi dothi.