Leviticus 17:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pajatu moyo wa cholengedwa chilichonse uli m'magazi mwake. Nchifukwa chake ndaŵauza Aisraele kuti, ‘Musadye magazi a cholengedwa chilichonse, pakuti moyo wa cholengedwa chilichonse uli m'magazi mwakemo. Aliyense wodya magazi adzachotsedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndiwo moyo wa nyama zonse, mwazi wake ndiwo moyo wake; chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israele, Musamadya mwazi wa nyama iliyonse; pakuti moyo wa nyama yonse ndi mwazi wake; aliyense akaudya adzasadzidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
chifukwa moyo wa cholengedwa chilichonse uli mʼmagazi ake. Nʼchifukwa chake ndinawawuza Aisraeli kuti, ‘Musamadye magazi a cholengedwa chilichonse, chifukwa moyo wa cholengedwa chilichonse uli mʼmagazi. Aliyense wodya magaziwo ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndiwo moyo wa: nyama zonse, mwazi wace ndiwo moyo wace; cifukwa cace ndinanena kwa ana a Israyeli, Musamadya mwazi wa nyama iri yonse; pakuti moyo wa nyama yonse ndi mwazi wace; ali yense akaudya adzasadzidwa.