Leviticus 17:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu aliyense wodya chinthu chofa chokha, kapena chojiwa ndi chilombo, ngakhale akhale mbadwa kapena mlendo, achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo, ndipo pambuyo pake adzakhala woyeretsedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo aliyense wakudya yakufa yokha, kapena yojiwa kuthengo, ngakhale ndiye wa m'dziko kapena mlendo, azitsuka nsalu zake, nasambe ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo adzakhala woyera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Munthu aliyense, kaya ndi mbadwa kapena mlendo, amene amadya chilichonse chofa chokha, kapena chojiwa ndi zirombo, achape zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Kenaka adzakhala woyeretsedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ali yense wakudya yakufa yokha, kapena yojiwa kuthengo, ngakhale ndiye wa m'dziko kapena mlendo, azitsuka nsaru zace, nasambe ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo adzakhala woyera.