Leviticus 17:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye kunena kuti Aisraele azitenga nyama zimene akadaphera kwina kwake, afike nazo pamaso pa Chauta kwa wansembe wokhala pakhomo pa chihema chamsonkhano, ndipo aziphere pomweko, kuti zikhale nsembe zachiyanjano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kotero kuti ana a Israele azidza nazo nsembe zao, zimene aziphera kuthengo koyera, kuti adze nazo kwa Yehova, ku khomo la chihema chokomanako, kwa wansembe, ndi kuziphera nsembe zoyamika za Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Izi zili choncho kuti Aisraeli azibwera ndi nyama zawo za nsembe zimene akanaphera ku malo kwina kulikonse. Aisraeli azibwera nazo nyamazo kwa Yehova, kwa wansembe wokhala pa khomo la tenti ya msonkhano ndipo aziphere pomwepo kuti zikhale nsembe za chiyanjano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kotero kuti ana a Israyeli azidza nazo nsembe zao, zimene aziphera kuthengo koyera, kuti adze nazo kwa Yehova, ku khomo la cihema cokomanako, kwa wansembe, ndi kuziphera nsembe zoyamika za Yehova.