Leviticus 18:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Usagone ndi mkazi ndiponso ndi mwana wamkazi wa mkaziyo, ndipo usagone ndi mwana wamkazi wa mwana wake wamwamuna, kapena mwana wamkazi wa mwana wake wamkazi. Amenewo ndi thupi lake la mkaziyo, ndipo kuteroko nkuchita chinthu choipa kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Usamavula mkazi ndi mwana wamkazi wake; usamatenga mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wake, kapena mwana wamkazi wa mwana wamkazi wake kumvula; ndiwo abale; chochititsa manyazi ichi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Usagonane ndi mkazi ndiponso mwana wake wamkazi. Usagonane ndi mwana wamkazi wa mwana wake wamwamuna, kapena mwana wamkazi wa mwana wake wamkazi. Amenewo ndi thupi limodzi ndi mkaziyo. Kutero ndikuchita chinthu choyipa kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Usamabvula mkazi ndi mwana wamkazi wace; usamatenga mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wace, kapena mwana wamkazi wa mwana wamkazi wace kumbvula; ndiwo abale; cocititsa manyazi ici.