Leviticus 18:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma inuyo mutsate malamulo anga ndi kuchita zimene ndikukulamulani. Musachite chilichonse mwa zonyansazi, ngakhale inu mbadwanu kapena mlendo wokhala pakati panu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma inu, muzisunga malemba anga ndi maweruzo anga, osachita chimodzi chonse cha zonyansa izi; ngakhale wa m'dziko ngakhale mlendo wakugonera pakati pa inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma inu mukasunge malangizo ndi malamulo anga. Mbadwa ndiponso alendo amene akukhala pakati panu asakachite china chilichonse cha zinthu zonyansazi,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma inu, muzisunga malemba anga ndi maweruzo anga, osacita cimodzi conse ca zonyansa izi; ngakhale wa m'dziko ngakhale mlendo wakugonera pakati pa inu;