Leviticus 18:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musamachita zimene amachita anthu a ku Ejipito kumene munkakhala kuja, ndiponso musadzachite zimene amachita anthu a ku Kanani kumene ndikukufikitsaniko. Musatsate miyambo yao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Ejipito, muja munakhalamo; musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Kanani kumene ndipita nanuko, nimusamayenda m'malemba ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musamachite zomwe amachita anthu a ku Igupto kumene munkakhala kuja, ndiponso musamachite zomwe amachita anthu a ku Kanaani kumene ndikukupititsani. Musatsatire miyambo yawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamacita monga mwa macitidwe a dziko la Aigupto muja munakhalamo; musamacita monga mwa macitidwe a dziko la Kanani kumene ndipita nanuko, nimusamayenda m'malemba ao.